Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Mpingo wa Katolika Uyenda Njira ya Mtanda 

 

Mpingo wa katolika mdziko muno komanso mipingo ina ya chikhristu pa dziko lonse lero yachita mwambo wa njira ya mtanda ngati njira imodzi yokumbukira masautso a ambuye yesu khristu.

Mwambowu umachitika chaka chilichonse tsiku la chisanu loyera pambuyo pa nyengo ya Lent.

Mwa zina, mu arkidayosizi ya mpingo wa katolikaya Blantyre, arkiepiskopi wa arkidayosiziyo Ambuye Thomas Luke Msusa ndi omwe anatsogolera mwambowu.

Kudzera pa mwambowu iwo apempha anthu mdziko muno kuti pamene akukumbukira masautso a Ambuye Yesu akhale okondana.

Mu dayosizi ya Zomba mwambowu unachitika kudzera mu mgwirizano wa mipingo ya katolika komanso Anglican ndipo ma episkopi a mipingoyi Ambuye George Desmond Tambala komanso Ambuye Brighton Malasa ndi omwe anatsogolera mwambowu.

Ndipo mu arkidayosizi ya Lilongwe mwambowu unachitika ku Maula Cathedral ndipo omwe anatsogolera ndi bambo Odvancio Kapingaomwe ndi bambo mfumu a Maula parishi.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices