Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Papa Achita Chotheka Kuthetsa Nkhondo Mdziko la Venezuella 

 

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati achitapo kanthu pofuna kuthetsa nkhondo ya pachiweniweni yomwe ikuchitika mdziko la Venezuela.

Papa amalankhula izi lamulungu pa bwalo la St Peter’s ku likulu la mpingowu ku Vatican.

Iye wapempha boma ndi anthu onse a mdzikolo kuti apewe zamtopola pofuna kulemekeza maufulu a anthu amene akupitilirabe kuphedwa, kuvulazidwa komanso kumangidwa.

Papa wati ali mu chisoni limodzi ndi mabanja onse a anthu omwe akhudzidwa ndi nkhondoyi komanso apitiriza kupemphelera dzikolo kuti likhale la mtendere ndi lopereka mphamvu ku anthu pa kayendetsedwe kake.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican zipani zotsutsa boma mdzikomo zikufuna kuti mdzikolo mukhale chisankho cha Pulezidenti komanso anthu 1 hundred omenyera maufulu a anthu omwe anamangidwa atulutsidwe.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices