Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Atolankhani Awayamikira Kamba Kovumbulutsa Zinthu Zobisika 

 

Atolankhani m’dziko muno awayamikira kamba kodzipereka pa ntchito zofalitsa mauthenga othandiza pa chitukuko cha miyoyo ya anthu m’dziko muno.

Ena mwa anthu omwe athilira ndemanga pa za momwe ntchito za atolankhani zakhala zikuyendera m’dziko muno ndi omwe anena izi lero pa 3 May lomwe ndi tsiku lokumbumbukira za ufulu wa atolankhani pa dziko lonse (World Press Freedom Day).

Popitiliza ndi ndemanga zawo anthu-wa ati atolankhani athandiza kubvumvulutsa zinthu zina zomwe zinali zobisika kuti ziwonekere poyera monga kusakazika kwa chuma cha boma ndi zina zambiri, zomwe zikusonyeza poyera kuti atolankhani m’dziko muno akudzipeleka pa ntchito yawo.

Pa 3 May chaka chili chonse, dziko la Malawi ndi maiko pa dziko lonse lapansi amakumbukira ufulu wa atolankhani. Mwambo okondwerera tsikuli mdziko muno chaka chino, uchitika loweruka likudzali mu mzinda wa Lilongwe komwe mwazina, atolankhani akasankha atsogoleri a bungwe la atolankhani la Media Institute of Southern Africa (MISA) Malawi Chapter omwe adzayendetsa bungweri kwa zaka zitatu zikudzazi.

Wapampando wabungwe la MISA Malawi Chapter Thom Khanje wati atolankhani ali ndi ufulu umene umachokera mu malamulo a dziko lino mu magawo 34, 35, 36 pomwe amapereka ufulu kwa mzika ya Malawi kuyankhula zakukhosi kwake pa zinthu zomwe zikuwakhudza. Khanje, wapitilira kunena kuti ndi magawo omwewa amene amapatsanso mphamvu ndi ufulu anthu otola ndi kulemba nkhani kuti alembe nkhani pa zochitika mdziko mwa ufulu ndi mosaopsyezedwa.

Pamene amavomereza kuti ufulu wa atolankhani ulipo, khanje wadandaula kuti boma likumagwiritsa ntchito nthambi zake kusokoneza ufulu wa atolankhaniwu.

Pofotokoza ngati boma la Malawi lakwanitsa kupereka ufulu kwa atolankhani monga momwe malamulo oyendetsera dziko lino anenera, nduna ya zofalitsa nkhani a Nicholas Dausi ati boma lachita zotheka powonetsetsa kuti atolankhani ali ndi ufulu onse pa ntchito yawo.

Pa madandaulo oti boma likugwiritsa ntchito nthambi za boma monga MRA ndi MACRA posokoneza ufulu ofalitsa nkhani, a DAUSI atsutsa izi ponena kuti ndi udindo wa nthambi-zi kuonetsetsa kuti malamulo a zofalitsa nkhani akutsatidwa Pamene zokonzekera za mwambo wa chaka chino okondwerera ufulu wa atolankhani zikufika kumapeto, anthu omwe akukapikisana pa udindo wa wapampando wa bungwe la MISA Malawi, Tereza Ndanga komanso Frank Phiri alonjeza atolankhani kuti ndiokonzeka kukweza ufulu olemba nkhani ngati atasankhidwa pa udindowu.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices