Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Akhristu Apemphelere Mtendere 

 

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu a mpingowu kuti apempherere mtendere pa dziko lonse pansi.

Malingana ndi malipoti a wayilesi ya Vatican Papa Francisco wapeleka pempholi lamulungu pa bwalo la St Peter’s Square ku Vatican pomwe amalankhula kwa anthu omwe anasonkhana pa bwaloli.

Iye wati m’mapemphero a kolona a mwezi uno wa May akhristuwa akhale akupempherera mtendere pa dziko la pansi monga momwe Mayi Maria wa ku Fatima anapemphera. 

Kumathero a sabata ino Papa Francisco akuyembekezeka kupita ku Fatima mdziko la Portugal komwe akakhale nawo pa mwambo okondwelera kuti patha zaka 100 chiwonekereni Amayi Maria ku malowo.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices