Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Akuba Aba ku Parishi ya Ntcheu 

 

Anthu anayi omwe sakudziwika aba katundu osiyanasiyana  ku parishi ya mpingo wa katolika ya Ntcheu mu dayosizi ya Dedza.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’boma la Ntcheu Sub-Inspector Hastings Chigalu wauza Radio Maria Malawi kuti anthuwa aba foni ziwiri za mmanja za bambo mfumu a parishiyo Bambo Atanazio Manyenga, makina a computer komanso ndalama zoposera K163,000.

“Anthuwa anakwera mpanda ndipo anamangilira mlonda komanso bambowa ndi ukonde,” anatero Sub-Inspector  Chigalu.

Sub-Inspector Chigalu wati anthuwa akagwidwa akawonekera ku bwalo la milandu ndi kukayankha mlandu  wakuba mwopseza zomwe ndi zotsutsana ndi gawo 301 loweruzira milandu.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices