Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Chiwerengero cha Anthu Opezeka ndi Kachilombo ka HIV Chatsika Mdziko la Malawi 

 

Bungwe la National Aids Commission NAC lati ndi lokondwa kamba koti chiwerengero cha anthu omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV mdziko muno chikutsika.

Mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli a Amidu Tung’ande ati kutsika kwa chiwerengerochi kwadza kamba koti anthu ambiri mdziko muno tsopano azindikira mmene angapewere matendawa.

“Padakali pano zikuwonetsa kuti anthu ambiri azindikira kuyipa komanso kapewedwe ka matendawa zomwe zikuchititsa kuti chiwerengerechi chitsike,” anatero a Tung’ande.

Iwo ati komabe ndi kovuta kuti dziko la Malawi likhale ndi chiwerengero chenicheni cha anthu omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matendawa kamba koti anthu ambiri  sapita kukayezetsa magazi.

A Tung’ande ayamikira mafumu kamba kothetsa zina mwa zikhalidwe zamakolo zomwe zimakolezera kufala kwa kachilombo koyambitsa matendwa.

“Zikhalidwe monga kulowa kufa, chokolo ndi zina zambiri zakhala zikulolezera kufala kwa kachilombo ka HIV choncho tiyamikire mafumu kamba ka ntchito yabwino yomwe akugwira,” anatero a Tung’ande.

Malinga ndi malipoti mu chaka cha 2010 kafukufuku amasonyeza kuti anthu khumi mwa 1 hundred aliwonse ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ndipo mu chaka cha 2016/2017 kafukufuku amasonyeza kuti anthu asanu ndi atatu mwa 1 hundred ali ndi kachilomboka.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices