Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Sister Maloya a Chipani cha SBVM Ayikidwa Mmanda 

 

Mwambo woika m’manda thupi la malemu sister Patricia Maloya chipani cha Atumiki a Maria Virigo Woyera uchitika lero ku Maryview ku Nguludi m’boma la Chiradzulu.

Malinga ndi a ku likulu la chipani-chi sister Maloya amwalira dzulo ndipo iwowa anabadwa pa 11 January chaka cha 1964 m’mudzi mwa Chirambe kwa mfumu yaikulu Mwambo m’boma la Zomba ndipo anachita malumbiro awo oyamba pa 8 December chaka cha 1986.

Mu nthawi ya moyo wao sister Maloya atumikilapo ku parishi ya Namulenga, ku nyumba ya a Episkopi a arch-dayosizi ya Blantyre ndi dayosizi ya Zomba, Maryview ku Nguludi, ku seminale ya Inter-Congregation Institute I.C.I m’boma la Balaka komanso ku seminale yaying’ono ya St Paul’s ku Mangochi.

Mwambowu uyamba ndi nsembe ya ukaristia yomwe atsogolelere ndi Arch episkopi wa Arch-dayosizi ya Blantyre Ambuye Thomas Luke Msusa kuyambira nthawi ya 10 koloko m’mawa.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices