Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Apempha Akhristu Kukhala Chitsanzo Chabwino 

 

Akhristu a m’phakati wa St Peters ku parish ya Sacred Heart mu dayosizi ya Zomba awalangiza kuti akhale chitsanzo chabwino komanso olimba pa chikhulupiliro chawo potengera momwe nkhoswe ya mphakati wawo Petro Woyera anali kuchitira.

Bambo Peter Mlomore, omwe ndi mkulu wa nthambi ya za chitukuko mu dayosiziyo, ananena izi pachaka cha nkhoswe ya mphakatiwu , komwenso akhristuwa amachita chaka choti mphakatiwu wakwanitsa zaka 27 chiukhadzikitsileni. Bambo Mlomore analimbikitsa akhristuwa kuti akhale olimba pa chikhulupiliro chawo komanso olimbikila pa ntchito zotukula mpingo wawo.

A Ellina Mwepeta omwe ndi m’modzi mwa atsogoleri a mphakatiwu anati akhristu aphakatiwu akhale ogwirizana kuti athe kudzidalira paokha.

Mwambowu unali wokumbukila nkhonswe ya mphakatiwu, Petro Woyera, komanso kukumbukila kuti mphakatiwu wakwanitsa zaka 27 chiukhanzikitsileni.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices