Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Apempha Ansembe Kudzipereka pa Utumiki Wawo 

 

Ansembe mu dayosizi ya Mangochi awapempha kuti akhale odzipereka pa utumuki wawo komanso adzisamalira katundu osiyanasiyana yemwe amagwiritsa ntchito.

Polankhula pambuyo pa msulo wa ansembe omwe dayosiziyo inakonza, Epsikopi wa dayosiziyi Ambuye Montfort Stima ati msulowo wathandiza ansembe m’dayosiziyo kuzindikira ubwino woteteza ana, kayendetsedwe ka bwino ka chuma cha mpingo komanso malamulo omwe ansembe amayenera kutsatira pamene akugwira ntchito zawo. Ambuye Stima anapempha ansembewa kuti adzitsata bwino malamulo oyendetsera ma parish omwe akugwiramo ntchito ndi cholinga chofuna kupititsa patsogolo utumiki wawo.

M’modzi mwa ansembe omwe amachita nawo msulowo bambo Chipondeponde ati msulo umenewu wathandiza ansembewa kuzindikira zakufunika kotetezera ufulu wa ana komanso anaunikira mfundo zina zofunika pa kayendetsedwe ka chuma chomwe chimapezeka m’malo amene ansembewo akugwira ntchito. Iwo ati aphunziranso zakufunika koteteza ndi kugwiritsa ntchito bwino katundu wa mpingo.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices