Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Apempha Gwirizano Pofuna kulimbana ndi Matenda a EDZI 

 

Anthu mdziko muno ati akuyenera kugwirana manja polimbana ndi kufala kwa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi komanso kupewa mchitidwe wosalana.

Polankhula ku mwambo woyatsa makandulo pokumbukira anthu omwe anamwalira ndi matenda a Edzi m’dera la Kachulu mfumu yaikulu Mwambo m’boma la Zomba, wachiwiri kwa wapampando wa khonsolo ya boma la Zomba Khansala William Likhusa ati ino si nthawi yakuti anthu azisalana chifukwa cha matenda a Edzi, koma akuyenera kuwonetsetsa kuti akugwira ntchito yolimbana ndi kufala kwa matendawa. Iwo alimbikitsa anthu m’dziko muno kuti akuyenera kugwirana manja ndi kuthandizana ndi cholinga chofuna kulimbana ndi kufala kwa mtenda imeneyi.

Mkulu woona za matenda a Edzi ndi Kadyedwe kabwino m’boma la Zomba a Chris Nawata ati boma la Zomba likutsatira ndondomeko zomwe boma la dziko lino linakhazikitsa pa ntchito yolimbana ndi matenda a Edzi kuti pofika mu chaka cha 2020 kufala kwa mliriwu kudzakhale kutatha. A Nawata ati pakadali pano boma la Zomba lakwanitsa kuchepetsa kufala kwa amatendawa kamba ka gwirizano omwe ulipo pakati pa ofesi yawo ndi anthu onse okhala m’boma la Zomba.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices