Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Maphunziro A M’mera Mpoyamba ndiofunika Kwa Ana. 

 

Bungwe la Future Vision Ministry lapempha makolo a mdera la Sub T/A Ngwelero m’boma la Zomba kuti azikhala ndi chidwi chotumiza ana awo sukulu za m’mera mpoyamba.

Mkulu wa bungweli a Newton Sindo ndi omwe anena izi pa sukulu ya m’mera mpoyamba ya pa Chinangwa Community Based Care pa mwambo wopeleka ma Certificate 60 kwa ana omwe afika pa mulingo woyamba maphunziro awo kusukulu za pulaimale.

A Sindo ati kutumiza ana ku sukulu za m’mera mpoyamba kumathandiza kuti anawa akapita ku sukulu za pulaimale asamakavutike koma kumachita bwino.

Polankhulapo mfumu  Namboya ya mdelaro nayo inathokoza bungweli kaamba ka chilimbikitso cha maphunzirowa kwa ana a m’bomalo. 

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices