Radio Maria Malawi

 

Amayi Awapempha Kuti Azithandiza Amayi Anzawo Ovutika. 

 

Amayi a mpingo wakatolika awapempha kuti adzipereke pa ntchito yothandiza amayi anzawo omwe akukomana ndi mavuto osiyanasiyana m’dziko muno.

Mkazi wa wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino , mayi Mary Chilima , ndi omwe anena izi ngati mlendo wolemekezeka pa mwambo wotsekulira msonkhano wa bungwe la amayi achikatolika la Catholic Women Organisation (CWO) mu arch-dayosizi ya Lilongwe. 

Mayi Chilima ati amayi akuyenera kumathandiza amayi anzawo pamavuto osiyanasiyana ndi kuti nawo azitha kukhala m’moyo wosangalala monga ena akukhalira.

Polankhulanso wapampando wa bungwe-li mu Ark- Dayosizi-yo  mayi Anita Kaliwu  anati bungwe-li  mu Ark- Dayosizi-yi lipitiliza kudzipeleka pa ntchito zothandiza amayiwa kudziwa luso la ntchito za manja, zomwe zithandize kuti azitha kupeza thandizo pa zosowa zawo mosavuta.

Mwambo wotsekulira msonkhano wa bungwe la amayi mu mpingo wakatolika mu arch-dayosizi ya Lilongwe unachitika pa 10 august 2017. 

Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices