Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Dr Chilima Alimbikitsa Za Mpingo Wodzidalira . 

 

Akhristu a mpingo wakatolika mu dayosizi ya Mangochi awapempha kuti apitilize kudzipereka pothandiza mpingo-wu molowa manja .

Wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino Dr Saulosi Chilima walankhula izi ngati mlendo wolemekezeka ku mwambo wa chaka chokondwelera nkhoswe ya dayosizi-yi. 

Pamenepa Dr Chilima ati akhristu a mpingo wakatolika mu dayosiziyi akuyenera kuti avale zilimbe pothandiza mpingo-wu molowa manja ndi modzipereka kamba koti tsopano mpingo-wu uli  m’manja mwawo chifukwa azungu omwe amathandiza mpingowu anabwelera kwawo. 

Mwambo wa chaka cha nkhoswe ya dayosizi ya Mangochi chinayamba ndi mwambo wa msembe ya misa yomwe anatsogolera ndi a episikopi a mpingo-wu mu dayosizi-yi  olemekezeka Ambuye Montfort Stima.

Mwazina akhristu-wa ku mwambo-wu athandizanso dayosizi yawo kudzera mu kugulitsa katundu wosiyanasiyana amene anabweletsa ndi cholinga chofuna kupeza ndalama zothandizira ntchito za dayosizi-yo.              

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices