Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Awapempha Kuti Azikhala Ndi Chidwi Chotsatira Bwino Chiphunzitso Cha Mpingo 

 

Mamembala a bungwe la Young Christian Workers (YCW) mu dayosizi ya mpingo wakatolika ya Zomba awapempha kuti azikhala ndi chidwi chotsatira bwino chiphunzitso cha mpingo wawo zomwe zingawathandize kuti akhale ozama pa chiphunzitso cha mpingo-wu.

 

Bambo Cosmas Namphimba, omwe akutumikira ku Seminale yayikulu ya mpingo wakatolika ya St Peters, ndi omwe anena izi pakutha pa  m’bindikiro wa masiku awiri wa uzimu , pakati pa mamembala a bungwe-li mu dayosizi ya Zomba.                        

Mbindikiro-wu unachitikira ku parish ya Namitembo, ndipo unayamba pa 6 ndikutha pa 7 October 2017. 

Polankhulanso a Friday Kalua m’modzi mwa achinyamata a YCW omwe achita nawo m’bindikiro-wu anati ndi okondwa ndi zimene aphunzira mmasiku a mbindikirowu ndipo zawathandiza kukhala akhristu olimba  

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices