Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Akhazikitsa Komiti Pofuna Kupeza Gwero La Moto Womwe Unatentha Police Secondary School 

 

Potsatira ngozi ya moto womwe wa sakaza katundu ndi nyumba yogona ophunzira pa Police Secondary School mu m’zinda wa Zomba, adindo okhudzidwa ndi nkhani-yi akhazikitsa komiti yofuna kupeza gwero la ngozi-yi.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’chigawo chaku m’mawa kwa dziko lino Inspector Joseph Sauka wauza Radio Maria Malawi kuti mwa zina komiti-yi, yomwe yapangidwa ndi nthumwi zochokera pa sukuluyi, apolisi, a ESCOM, ndi a kuofesi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi, ndinso a ku khonsolo ya mzindawu ithandizanso kupeza mulingo wa katundu amene wasakazika pa ngozi-yi.  Ngozi ya kupsya kwa nyumba yogona ophunzira pa Police Boys Secondary School mu m’dzinda wa Zomba, yachitika dzana usiku  ndipo yakhudza ophunzira 139 a pasukulu-yi.

Polankhula mkulu wa ku ofesi yozimitsa moto ya Fire Brigade mu khonsolo ya mzindawu a Leodins Sendaluzi wati anthu mukhonsoloyo akuyenera kumadziwitsa ofesi-yi mwansanga kudzera pa nambala ya 999 pogwilitsa ntchito nambala ya TNM kapena MTLkamba koti ndi yaulere.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices