Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Apempha Boma Kusintha Zina Mwandondomeko Zake Zoyendetsera Dziko. 

 

chipani cholamula cha Democratic Progressive(DPP), kuti chikonze mavuto omwe anthu akukumana nawo m’dziko muno.

Polankhula ndi Radio Maria Malawi mu m’dzinda wa Blantyre a Hamphrey’s Mvula ati chipani chomwe chimakhala chikulamula m’dziko, chimayenera kumakwanilitsa kutumikira anthu pa zosowa zawo nthawi zonse. Iwo anena izi potsatira kusachita bwino kwa chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) pa chisankho chachibwereza chomwe chinachitika pa 17 October, 2017 m’madera ena a dziko lino.

M’mawu awo a Mvula atinso nthawi yakwana yoti anthu azikhala ndi nthawi yopanga maganizo azofuna zawo mwaufulu posatengera kusiyana kwa zipani ndipo apemphanso chipani chalamula mdziko muno kuti tsopano ndi nthawi yoti akonze zina mwa njira zomwe zapangitsa kuti chisachite bwino pa chisankho cha chibweleza chomwe chinachitika masiku apitawa.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices