Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Anjatidwa Kaamba Kopezeka ndi Mankhwala a Chipatala 

 

Apolisi m`boma la Mwanza akusunga mchitolokosi mayi wina wa zaka 36 zakubadwa kaamba komuganizira kuti wapezeka ndi mankhwala a chipatala popanda chilolezo.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’boma la Mwanza, Sergeant Edwin Kaunda, wati apolisi a pa chipata cha Mwanza amanga a Patricia Ntchepa lamulungu pa 26 November 2017 pamene amachita chipikisheni mu bus yomwe mayiyu anakwera ya kampani ya Monorurama yomwe imapita mdziko la South Africa.

Atafufuza mu chikwama cha mayiyu, apolisiwo anapeza mankhwala ndipo atafunsa mayiyu analephera kupelekera umboni wokwanira okhudzana ndi mankhwalawo.

Mankhwalawa anali mapilisi 1000 a Buffen, Makapusolo 1000 a Doxycline, Makapusolo 1000 a Indocin, Mapilisi 1000 a Bactrim, Mapilisi 500 a Penicillin, Mapilisi 696 a LAA ndi mapaketi ena okwana 1000.

Pakadali pano mayiyu ali m’manja mwa apolisi ndipo akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedswapa ndi kukayankha mlandu opezeka ndi mankhwala a chipatala popanda chilolezo.

Patricia Ntchepa amachokera m`mudzi mwa Gulufu kwa mfumu yaikulu Kunthembwe m`boma la Blantyre.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices