Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Papa Apempha Maepiskopi Atumikire Mulungu Modzipereka 

 

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wapempha ma episkopi a mpingo wa katolika mdziko la Myanmar kuti apitirize kutumikira anthu mdzikolo pofalitsa uthenga wa mulungu modzipereka.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa amalankhula izi pa mkumano wake ndi ma episkopi 22 ampingowu mdzikomo omwe unachitikira ku Yangon’s Cathedral pamene akupitiriza kucheza ndi akhristu a dzikolo.

Papa wati ngakahale ma episkopiwa akukumana ndi zovuta mu utumiki wawo iwo akuyenerabe kutumikira mulungu mokondwa.

Dziko la Myanmar lili ndi ma arkidayosizi atatu komanso ma dayosizi khumi ndi atatu (13) ndipo wamkulu wa bungwe la maepiskopiwa ndi Ambuye Felix Thang.

Atamaliza mkumano ndi ma episkopiwa, papa anadalitsanso miyala ya maziko ya matchalitchi okwana 16, seminale yayikulu ya mdzikolo komanso nyumba ya nthumwi ya a papa mdzikolo.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices