Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Msonkhano wa AU, EU Uli Mkati ku Ivory Coast 

 

Msonkhano wa atsogoleri a m’bungwe la maiko a mu Africa la African Union AU komanso a ku Ulaya la European Union (EU),uli mkati mdziko la Ivory Coast.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, mfundo yaikulu yomwe atsogoleriwo akukambirana ndi  ya momwe angapititsire patsogolo miyoyo ya achinyamata, omwe malinga ndi kafukufuku, anthu 60mwa anthu 100 aliwonse m’maiko a mu Africa ndi a zaka zosapyola 25.

Pali chiyembekezo choti atsogoleriwo akambirananso mavuto omwe achinyamata akukumana nawo m’maiko a mu Africa, omwe akudza kaamba ka mavuto a zachuma komanso nkhondo.

Malipoti ati achinyamata mazanamazana a m’maikowa akhala akufa mnyanja ya Mediterrenian m’maulendo opita m’maiko aku Ulaya kuti akapeze ntchito zotukulira miyoyo yawo.

Masabata apitawa, maepiskopi a mpingo wa katolika m’maiko a mu Africa ndi Ulaya anayamikira mutu wa msonkhanowu chaka chino pokhudza za achinyamata omwenso wagwirizana ndi mutu omwe ma episkopiwa adzakambirane ku msonkhano wawo omwe udzachitikire ku likulu la mpingo wakatolika ku Vatican m’chaka cha 2018.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices