Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Achinyamata Azindikiritsidwe Ndondomeko Zoyendetsera Maboma Aang’ono 

 

Mabungwe osiyanasiyana awapempha kuti atenge mbali pozindikilitsa achinyamata ndondomeko zoyendetsera maboma ang’ono ndi cholinga choti akhale mzika zodalirika za dziko lino.

 

Mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya sekondale ya anyamata ya Zomba Catholic a Steven Bonifacendi omwe anena izipamtsutso omwe unakonzedwa ndi nthambi ya za maphunziro ku bungwe la mpingo wakatolika la Catholic Development Commission (CADECOM) omwe unachitikira kusukulu yasekondale ya atsikana ya St. Mary’s mu mzinda wa Zomba.

Iwo ati maphunziro amtunduwu ndiwofunika kwambiri kwa achinyamata kaamba koti amathandiza kuti adziwe m’mene zinthu zimayendera mdziko pankhani zachuma.

 

Polankhulapo m’modzi wa ophunzira ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor, Wezzie Mphulayemwenso anali m’modzi wa akatswiri omwe amaunika mtsutsowu anati achinyamata ambiri sakhala ndi umwini pa zitukuko za dziko kamba koti amasowa upangiri owazindikilitsa mmene ndondomeko zachuma zimayendera komanso mmene maboma ang’ono amagwilira ntchito zao.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices