Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Apolisi Anjatidwa Kamba Koba Makoponi 57  

 

Apolisi m’boma la Dowa amanga apolisi awiri a pa polisi ya Mponela m’bomalo, powaganizira kuti aba makuponi ogulira fetereza komanso mbeu ya boma yotsika mtengo mothandizidwa ndi munthu wina, yemwe pakadali pano akufunidwa ndi apolisi.

Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Richard Kaponda, watsimikizira Radio Maria Malawi kuti apolisiwo, ndi Sergeant Zakeyo Kadzakumanja wa zaka 34 zakubadwa ndi Sergeant Chipiliro Nazonse wa zaka 39zakubadwa.

Apolisi awiriwa akuti anaba makuponi 57 a ndalama zoposa 850 sauzande kwacha kwa a Joel Chrispin Hara, omwe amagwira ntchito ku kampani ya World Wide Wholesalers ku Mitundu.

Sergeant Zakeyo Kadzakumanja, ndi wa m’mudzi mwa Mvula kwa mfumu yaikulu Lukula m’boma la Kasungu, ndipo Chipiliro Nazonse ndi wa m’mudzi mwa Samala mdera la mfumu yaikulu Nsamala m’boma la Balaka.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices