Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Anthu Akhale Tcheru ndi Malungo-WHO 

 

Bungwe lowona za umoyo pa dziko lonse la World Health Organization (WHO), lachenjeza maiko kuti akhale tcheru ndi matenda a malungo pamene zikusonyeza kuti kupambana komwe kudalipo pogonjetsa matendawa kukutsika.

Mkulu owona za matenda a malungo ku bungweli Pedro Alonso, wauza wailesi ya BBC kuti uthengawu ukhale chenjezo lalikulu ku maiko omwe amakhudzidwa ndi matendawa, kaamba koti ntchito yolimbana ndi matendawa siili mchimake.

Malipoti a bungweli akusonyeza kuti chiwerengero cha padziko lonse cha anthu omwe anakhudzidwa ndi matendawa chaka chatha, chinakwera ndi 5 million, ndipo anthu 400 sauzande anamwalira, omwe ambiri mwa iwo anali ana a zaka zosapyola zisanu.

Nthambiyi yati nkhondo yolimbana ndi matendawa siikupita patsogolo, mwa zina, kaamba ka kunyalanyaza njira zopewera matendawa, monga kugona m’masikito oteteza ku udzudzu komanso kupopera mankhwala m’nyumba za anthu.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices