Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Praljak Amwalira Atamwa Poizoni mu Khothi 

 

Mmodzi mwa akuluakulu asanu ndi mmodzi omwe amaimbidwa milandu yokolezera nkhondo mdziko la Bosnia, wamwalira atamwa poizoni m’bwalo la milandu ku Hague mdziko la Nertherlands.

Mkuluyo,Slobodan Praljak,wamwalira, bwalo lamilandu pa dziko lonse la International Criminal (ICC), litatsimikiza  chigamulo choyamba chomwe lidapereka kwa mkuluyo, choti akakhale kundende kwa zaka makumi awiri.

Iye yemwenso panthawiyo anali mkulu wa asilikali, anamwa mankhwalawo mkhothi momwemo, pamene mulandu wake umaweruzidwa komaliza, atatsimikiziridwa kuti akakhala ku ndende kwa zaka zochuluka motere.

Praljak, yemwe wamwalira ali ndi zaka 72, wamwalirira kuchipatala komwe anamutengera atangomwa mankhwalawo.

Iye amamuimba mulandu okolezera nkhondo yomwe inali mdzikolo mzaka za 1992 mpaka 1995.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices