Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Thindwa Ayikira Kumbuyo Ganizo la Aphungu Otsutsa 

 

M’modzi mwa akatswiri pa nkhani za ndale mdziko muno Enerst Thindwa waikira kumbuyo ganizo la zipani zotsutsa boma motsogozedwa ndi chipani cha Malawi Congress (MCP) ponyanyala zokambirana ku nyumba ya malamulo kaamba ka kusapezeka kwa bilu yofuna kusintha kayendetsedwe ka chisankho mdziko muno.

Thindwa awuza Radio Maria Malawi kuti aphungu otsutsa, ali ndi ufulu onyanyala zokambirana ku nyumba ya malamulo, ngati akufuna kukakamiza boma kuti lichite zomwe akufuna.

Iwo adabwa ndi boma kaamba kosatekeseka ndi zomwe anthu ambiri mdziko muno, akufuna maka pofuna kusintha ena mwa malamulo akayendetsedwe ka chisankho.

A Thindwa ati ngakhale nthawi zina zimatheka aphungu a boma kumakambirana popanda otsutsa boma, nthawi zambiri zimasokoneza ufulu wa democracy.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices