Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Moto Utentha Chipatala cha Boma la Ntcheu 

 

Ntchito za pachipatala cha Ntcheu akuti zasokonekera kaamba ka ngozi ya moto umene wasakaza nyumba ndi zina pa chipatalachi.

Wofalitsa nkhani za pa chipatala-chi mayi Stella Kawalala ati akukhulupilira kuti ngozi-yi yomwe yachitika m‘mawa wa pa 3 mwezi uno, inachitika kaamba ka vuto la magetsi pa chipatalachi.

Padakalipano mkulu wa ku ofesi ya za umoyo pa chipatalachi Dr. Mike Chisema,wauza atolankhani a MANAkuti  ngoziyi sinakhudze makhwala a pa chipatalachi.

Padakalipano ntchito yowonkhetsa ndi kufuna kudziwa mulingo wa katundu amene wasakazika pangoziyi akuti ili mkati.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices