Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Dziko La Zimbabwe Likufufuza Momwe Grace Mugabe Anapezera PhD Yake 

 

Bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu mdziko laZimbabwelikuchita kafukufuku wofuna kupeza ngati mkazi wa mtsogoleri wakale wa dzikolo aGrace Mugabeanapeza certificate yake yaPhDmwachinyengo.

Malipoti a wailesi ya BBC, ati mayi Mugabeanapatsidwa certificate ya PhD ataphunzira ku sukulu ya ukachenjede kwa miyezi yochepa pamene zimafunika kuti munthu aphunzire zaka zingapo kuti alandirePhD.

Akuluakulu a bungweli mdzikomo ati alandira malipoti oti mayi Mugabe analandira certificate ya PhD kuchokera ku sukulu ya ukachenjede ya dzikolo ya University of Zimbabwe mchaka cha 2014 mwachinyengo.

Malipoti ati Grace Mugabe amaphimbidwa ndi mwamuna wake yemwe pa nthawiyo anali mtsogoleri wa dzikolo komanso mkulu wa sukulu za ukachenjede mdzikomo.

Grace Mugabe yemwe ankafuna kulowa m’malo mwa mamuna wake Robert Mugabe kukhala mtsogoleri wa dzikolo anakanika asilikali a dzikolo atalowelerapo pa mikangano yomwe imachitika mdzikomo zomwe zinachititsa kuti yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikolo a Emmerson Mnangagwaatenge ulamuliro wa dzikolo ngati mtsogoleri, zomwe zinathetsa zaka 37 za ulamuliro wa a Mugabe.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices