Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Alimbikitsa Anthu Kuganizira za Chitukuko cha Dziko Lino 

 

Wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Chilima wati nkofunika kuti anthu m’dziko muno ayambe kuganiza mwakuya ndi kupeza njira zabwino zomwe zingathandize pa ntchito zotukula dziko lino.

Polankhula pa mwambo wokhanzikitsa mulozo wa ntchito zomwe dayosizi ya mpingo wakatolika ya Zomba yakonza kuti izikwanilitsa mu zaka zisanu zikudzazi, Dr Chilima ati ndi okhutira ndi ntchito zomwe dayosiziyo yakonza kuti izikwanilitse muzakazi ndipo apempha akhristu amu dayosiziyo  kuti agwirane manja kuti ntchito zomwe zakonzedwazo zitheke. Iwo alimbikitsa akhristuwa kuti adziyamba kudzithandiza ndi kuzitukulu okha asanafunse chithandizo kwa anthu ena.

Ndipo episikopi a dayosiziyo Ambuye Gorge Desmond Tambala alimbikitsa akhristu mu dayosizi-yo kuti adzipeleke pa ntchito zotukula dayosiziyi ndi cholinga choti mapulani a ntchito zotukula dayosiziyo akwanilitsidwe. Ambuye Tambala ati zomwe zili mu mulozo umenewu zikuyenera kuchitikadi ndi cholinga choti dayosiziyo itukuke.

Mulozowo wakonzedwa ndi cholinga choika ntchito za chitukuko zomwe dayosizi ya Zomba ikufuna kupanga mu zaka zisanu zikubwerazi poyera komanso kuti akhristu eni azidziwe ntchitozo ndi cholinga choti adzitha kukonzekera bwino.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices