Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Apempha odwala Nthenda ya Khunyu kupita kuchipatala Mwansanga 

 

Makolo m’dziko muno, awapempha kuti azifulumira kukaonana ndi madotolo , ngati awona kuti ana awo akusonyeza zizindikiro za matenda a kugwa.

M’modzi mwa akulu-akulu ku bungwe lomwe limapeleka thandizo la matendawa m’dziko muno la National Epilepsy Association Of Malawi m’boma la Machinga a Jailosi Wachimwa, ndi omwe anena izi polankhula ndi mtolankhani wathu , amene amafuna kudziwa zambiri zokhudza ntchito za bungwe-li .

Iwo ati bungwe lawo likudzipereka kwambiri pa ntchito zothandiza anthu-wa , kotero kuti anthu onse amene ali ndi vutoli asamangokhala , koma kuti azilalandira thandizo kuchipatala, M’mawu awo iwo anati nthawi yakwana yoti makolo asamangolekerera akaona anawa koma azithamangira nawo kuchipatala akaona zizindikirozi kuti azikalandira thandizo loyenerera ndipo achenjeza makolo omwe ali ndi nchitidwe opita ndi ana awo kwa asing’anga akadwala mthendayi m’malo mwake iwo ati makolowa azifulumira kupita kuchipatala mwansanga. 

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices