Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Archdayosizi ya Lilongwe Ikhazikitsa Ntchito Yotolera Thandizo Lomangira Cathedral Yatsopano 

 

Akhristu a mpingo wakatolika mu Archdayosizi ya Lilongwe awapempha kuti agwirane manja pa ntchito yomanga cathedral yatsopano mu Archdayosiziyo.

Mkulu woona za chuma mu Archdayosiziyi bambo Gerald Kubetcha ndi omwe alankhula izi ndi Radio Maria Malawi pomwe loweruka archdayosiziyi ikhale ikukhazikitsa ntchito yotolera thandizo lofuna kupeza ndalama zomangira cathedral yatsopanoyi.

Bambo Kubetcha ati akhristu a mu Archdayosizi-yi akuyenera kuzindikira kuti ntchitoyi si ya akhristu a ku parishi ya Maula okha koma aliyense wopezeka mu dayosiziyi.

“Ntchito yotolera ndalama zomangira tchalitchi latsopanoli yagona pa mkhristu aliyense wa mu archdayosizi ino,”anatero Bambo Kubetcha.

Iwo ati Arch dayosizi ya Lilongwe yakhala yopanda cathedral kwa nthawi yaitali ndipo kuti tchalitchi  lomwe lakhala likugwiritsidwa ntchito ngati cathedral  linangosankhidwa koma ndi parishi chabe.

Bambo Kubetcha ati padakali pano ndalama zomwe zikufunika pa ntchitoyi sizinadziwike koma akufuna tchalitchili lidzakhale lolowa anthu osachepera 5 sauzande.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices