Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Athokoza Akhristu Kaamba Kozipeleka Pothandiza Mpingo 

 

Episikopi wa Arch-Dayosizi ya Blantyre, olemekezeka Ambuye Thomas Luke Msusa wayamikira akhristu a mpingo-wu mu Arch-Dayosizi-yi kamba kodzipeleka pa mwambo wa Dinner and Dance yomwe mpingo-wu unakonza pofuna kupeza ndalama zothandizira ntchito zake mu dayosizi-yi.

Ambuye Msusa alankhula izi pofotokozera mtolankhani wathu. Iwo ati kupanda kuti anthu sanadzipereke pothandiza mpingowu pa dinner and dance imeneyi sibwenzi mpingowu utakwanitsa kutolera ndalama zokwana 18 Million Kwacha zomwe zinapezeka pa tsikuli.  

M’mawu awo iwo anati pakadali pano mpingo wakatolika ndioziimira paokha kotero akhristu eni ake akuyenera kumatenga mbali kwakukulu pothandiza mpingowu ndipo anati mwabo umenewu wathandiza kwambiri kaamba koti ndalama zomwe zapezekazi zithandiza kwambiri kutumikira ansembe achibwadiri mu Dayosizi-yi makamaka akadwala zomwe ati sipakhalanso chovuta chilichonse kupeza thandizo kwa ansembewa. 

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices