Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Bambo Wafa Ali Mkati Mwa Makina Osakanizira Cement Mu Mdzinda Wa Lilongwe. 

 

Bambo wina wafa atalowa mkati mwa makina osakanizira cement a kampani ya Capital Food ku Kanengo mu m’dzinda wa Lilongwe.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi ku Kanengo a Salome Chibwana ati munthuyi ndi Geleson Chinkhuzi ndipo analowa mkati mwa makinawo kuti akakonzemo, koma mwatsoka bwana wa kampaniyo akuti analamulanso wogwira ntchito wina kuti akayatse makinawo zomwe zapangitsa kuti mkuluyi avulale modetsa nkhawa.

Atazindikira za ngoziyi bwanayo akuti anatengera mkuluyi kuchipatala cha Kamuzu Central komwe wakamwalilira .

Malipoti a kuchipatala asonyeza kuti mkuluyi wamwalira kamba kotaya magazi ochuluka. Malemu Geleson Chinkhuzi anali ochokera m’mudzi mwa Nyangala m’dera la mfumu yayikulu Dzoole m’boma la Dowa. 

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices