Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Dayosizi Ya Mangochi Ilimbikitsa Ana Kupewa Malungo 

 

Dayosizi ya mpingo wa katolika ya Mangochi kudzera mu nthambi yoona za umoyo ya Catholic Health Commission mu dayosiziyo yati ipitiriza kuphunzitsa ana njira zimene angapewere matenda a malungo.

Vicar General wa dayosiziyo yemwenso ndi wapampando wa nthambiyi, bambo Andrew Nkhata anena izi pa sukulu ya pulaimale ya Michongwe ku Ntaja m’boma la Machinga pa mwambo wa chionenetsero cha zaumoyo omwe nthambiyi inakonza.

Iwo ati kupatula edzi, nthenda ya malungo ikupha anthu ambiri maka chifukwa cha zizolowezi zina zosayenera.

Mwambowu unachitika pamutu woti “Kupewa Malungo Pa Kusintha Chikhalidwe Ndi Chizolowezi”.

Polankhulapo mlembi wamkulu wa nthambiyi mu dayosiziyi a Peterkins Chisoni anati matenda a malungo ndi owopsa ndipo ana akuyenera kuphunzitsidwa kapewedwe kake adakali achichepere.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices