Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Dziko La Japan Lipereka 112 Sauzande Dollars Zomangira Sukulu M’boma La Chiradzulu 

 

Boma la dziko la Japan lapereka ndalama zokwana 112 thousand 984 za America ku boma la dziko lino zothandizira kumangira sukulu ya sekondale yoyendera ya Chikangulu m’boma la Chiradzulu.

Polandira thandizoli ku ofesi ya kazembe wa mdziko la Japan mu mzinda wa Lilongwe nduna ya zamaphunziro, sayansi ndi luso la makono Dr. Emmanuel Fabiano anayamikira boma la dzikolo kaamba ka thandizolo ndipo yati ikukhulupilira kuti dziko la Japan lipitiriza kuchita zinthu za mtunduwu ndi cholinga choti dziko la Malawi litukuke.

Polankhulapo kazembeyu Kae Yanagisawa wati akukhulupilira kuti thandizolo ligwira ntchito moyenera komanso kuti anthu a mderalo asamalira chitukukochi.

Iye wati dziko la Japan lipitiliza kutukula dziko la Malawi pa nkhani ya maphunziro kaamba koti ndi chinthu chimodzi chomwe chikulimbikitsidwa mdziko muno.

Pamenepa Yanagisawawapempha anthu omwe akuyang’anira ntchito yomanga sukuluyi kuti achite changu pa ntchitoyi.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices