Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Migwirizano Ina Ikhumudwitsa Papa 

 

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati ndi wokhumudwa ndi migwirizano yomwe imakhalapo pakati pa maiko omwe ndi amphamvu komanso otukuka pa chuma.

Papa Francisco wati mgwirizano pakati pa maiko a America ndi Russia, China ndi North Korea komanso Russia ndi Syria ndi ina mwa migwirizano yomwe ndi yoipa kwambiri kamba koti mfundo zomwe mgwirizano ngati imeneyi imakambilana imasaukitsa maiko omwe siwotukuka pa chuma komanso imabweretsa kusamvana pakati pa maiko osiyanasiyana. Polankhula asanakumane ndi atsogoleri omwe maiko awo ali m’gulu la gwirizano wa maiko otukuka kwambiri pa chuma pa dziko lonse la G20 Papa Francisco wati mfundo zomwe mgwirizanowo umatsatira zikubweretsa mavuto m’maiko osauka zomwe ati zikuchulukitsa mchitidwe wa anthu othawa m’maiko awo. Papa wapempha maiko otukukawa kuti athandize maiko osauka kutukula chuma cha m’maiko awo.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices