Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Mmodzi mwa Oyang’anira Chisankho Mdziko la Kenya Atula Pansi Udindo 

 

Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe loyendetsa chisankho mdziko la Kenya la Independent Electoral and Boundaries Commission (IEBC) watula pansi udindo wake patangotsala masiku ochepa kuti dzikolo lichititse chisankho cha chibwereza cha pulezidenti.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, mayi Roselyn Akombe wati watula pansi udindo wake kaamba koti bungwe loyendetsa chisankholo likugwira ntchito pansi pa ndale ndipo likulephera kupanga ziganizo zomveka bwino pa lokha.

Mayiyu amene padakali pano ali mdziko la America wati wachoka mdzikolo pofuna kuteteza moyo wake kaamba koti wakhala akulandira mauthenga omuopseza.

Sabata yatha mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma dzikolo a Raila Odinga analengeza kuti sapikisana nawonso pa chisankho cha chibwerezachi chomwe chikuyembekezeka kuchitika pa 26 mwezi uno.

Bwalo lalikulu la milandu la dzikolo linayimitsa kaye zotsatira za chisankho cha pulezidenti chomwe chinachitika mdzikolo pa 18 August chomwe chinapeza kuti mtsogoleri wa dzikolo a Uhuru Kenyatta ndi omwe anapambana ati kaamba koti panali zina zomwe sizinayende bwino.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices