Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Papa Apempha Akhristu Akhale Otumikirana 

 

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu kuti akhale othandizana komanso otumikirana pakati pawo.

Papa amalankhula izi ku ndende ina mu mzinda wa Rome pa tsiku lachinayi loyera pomwe anakasambitsa mapazi akayidi  ku ndendeyi.

Iye wati akhristu akuyenera kukhala odzichepetsa monga momwe Mulungu mwini alili.

Pa mwambowu mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu anasambitsa mapazi a akayidi khumi ndi anayi, ndipo mwa akayidiwa m’modzi anali wa chipembedzo cha chisilamu ndipo atatu anali amayi.

Papa anayamba kuchita izi mu chaka cha 2013 atangosankhidwa kumene pa udindowu pomwe koyamba anasambitsa mapazi a amayi ndi a anthu a chipembedzo cha chisilamu.

Mu chaka cha 2014 Papa anakachita mwambowu kumalo ena osungirako anthu olumala pomwenso mwa anthu omwe anawasambitsa mapazi anali amayi.

Ndipo mu chaka cha 2015 Papa anakatsukanso mapazi a akayidi a pa ndende ina ya mdzikolo pomwe chaka chatha anatsuka mapazi a anthu othawa kwao omwe mwa anthuwo panali a zipembedzo za chisilamu ndi Hindu komanso a mpingo wa Orthodox.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices