Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Papa Atsekulira Malo Ochapira a Ulere 

 

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Fransisco watsegulira malo omwe anthu ovutika  azikagwilitsa ntchito akafuna kuchapa komanso kusitilako zovala mwa ulele mu mzinda wa Vatican mdziko la Italy.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa wachita izi pofuna kuchepetsa mavuto omwe anthu ovutika amakumana nawo mdzikolo ndipo ati izi zachitika mothandizidwa ndi bungwe la Whirl Pool.

Bungweri ati lapeleka makina ochapila zovala asanu ndi imodzi (6), makina oumitsila zovala asanu ndi imodzi (6) ndinso ma Iron.

Ndipo ati posakhalitsapa likhadzikitsanso malo ometera komanso chipatala chomwe chizithandiza anthu-wo.

Awa ndi malo achiwiri omwe mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu watsegulira potsatila kutsegulidwanso kwa malo ena omwe anatsegulidwa m’zaka ziwiri zapitazo ndipo ati cholinga chake ndikufuna kuthandiza anthu omwe ndi ovutika.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices